Back to Home Page of CD3WD Project or Back to list of CD3WD Publications

PREVIOUS PAGE TABLE OF CONTENTS


Appendix I - Text for Chichewa/Nyanja individual reading

Mfumu Mitulo atacoka pamudzi paja nyakwawa Kameta ndi anthu ake pamodzi ndi ena ocokera m'midzi yozungulira, anagundika nayo nchito youmba ncherwa zomangira sukulu.

Azimai ndiwo amabweretsa madzi ndi udzu wophimba pancherwa, pamene anyamata anali kuthamanga ndi zikombole. Azibambo ndiwo anali m'nkhando kumaponda dothi. Panthawiyi amuna ena anali kudula nkhuni zodzatenthera ncherwa.

Ncherwa zittakonzedwa, nyakwawa Kameta anauza Bambo Jamu omwe amadziwa kamangidwe ke nyumba za ncherwa kuti akayambeko kukumba maziko a sukulu.


PREVIOUS PAGE TOP OF PAGE